Kodi corona ndichiyani ndipo ndingachite chani pa nkhaniyi?

Corona ndi kachilombo kakang'ono kamene sikangawoneke ndi maso athu kamene kakhoza kufalikila komanso kupereka matenda Ku anthu. Corona amawonetsa zizindikiro monga chimfine, kupuma mobanika, kutentha thupi, komanso kumva kupweteka muthupi. Corona amagwiranso kwambiri mu ziwalo zomwe mumadutsa mpweya mthupi lathu. Amaperekanso zibayo za mumapapo ngati nthendayi yafika pachimake.

Aliyense akhoza kutenga corona. Anthu okalamba komanso amene amadwala matenda ena monga cancer ndi shuga amakhala pa chiopsezo chachikulu cha zizindikiro za corona akatenga kachilomboka.

Corona imafala kudzera mu mpweya umene munthu amene ali ndi kachilomboka akupuma, kutsokomola, kapena kuyetsemula. Kachilomboka kamalowa mu thupi la munthu kudzera pakamwa, mumphuno ndi mumaso. Tizilomboti tikalowa mu thupi timayamba kuswana kapena kuberekana ndipo timafalikira mu thupi lonse. Corona akhoza kukhala mu thupi la munthu masiku pafupifupi 14 asanawonetse zizindikiro za kudwala. Kotero anthu akhoza kukhala ndi Corona koma osadziwa ndipo akhoza kufalitsa kwa anthu ena.

Kachilomboka ka corona sikaphedwa ndi mankhwala aliwonse kapena chilichonse chochitika pakhomo. Ngakhale zilichoncho corona tikhoza kumupewa posakhudzana komanso kusamba mmanja ndi sopo pafupipafupi.

Tingapewe kachilomboka posamba mmanja ndi sopo komanso madzi abwino ngakhale mmanja mwathu muli moyera kale. Tisambe bwinobwino mpaka mkatikati mwa zala komanso mmanja kwa 20 seconds ndi sopo. Kusamba mmanja ndi sopo kumapha kachilombo ka corona kamene kangapezeke mmanja. Nthawi zonse tisambe mmanja tisanakonze chakudya komanso tikatha kukonza chakudya, tikachoka Kuchimbuzi, pa nthawi imene tikusamalira wodwala, pamene tamaliza kugwira ziweto, tikatha kutsokomola, kuyetsemula, kapena kumina.

Tipewe kugwira mu maso, mumphuno, ndi kukamwa tisanasambe mmanja. Manja amagwira zinthu zambiri zosiyanasiyana kotero akhoza kutenga kachilombo mosavuta ndipo manja omwewo akhoza kuyika kachilomboka kumaso kwathu, mumphuno, komanso kukamwa, kenaka kachilomboka kakhoza kulowa mthupi kutipangitsa ife kudwala.

Ndichinthu chofunikira kwambiri kupewa kukhudzana ndi munthu amene watentha thupi, kutsokomola, komanso amene akupuma mobanika. Tikamatsokomola kapena kuyetsemula nthawi zonse tiwonetsetse kuti tatseka kukamwa ndi kansalu kapena tissue. Tikatha kugwiritsa tissue tiwonetsetse kuti tataya malo oyenera. Tisamalavule penapaliponse tikakhala pagulu.

Tizitalikilana pafupifupi 1 metre ndi munthu amene akutsokomola kapena watentha thupi kapena kuyetsemula. Tipewe kukhudzana ndi wina aliyense amene watentha thupi kapena kutsokomola.

Ngati tikufuna kusamalira munthu amene watentha thupi, a kutsokomola, kapena kubanika popuma, tisaiwale kuvala zozitetezera kuti tisatenge kachilombo monga zophimba kukamwa ndi kumphuno. Komanso tizolowere kusamba mmanja pafupi pafupi.

Corona tingamupewe posakhudzana ndi anzathu. Corona komanso tizilombo tina tikhoza kufala popatsana moni wa mmanja kenaka manja omwewo kugwirira kumaso, mumphuno, ndi kukamwa. Kotero tikakumana ndi anzathu tisamapatsane moni wa mmanja, kukumbatirana, kapena kupyopyonana. Tikamapereka moni tizingokweza mkono kapena kugwedeza mutu. Ngati tikuganiza kuti mu dera lathu Corona alimo, tikhale pakhomo osayendayenda popewa kukhudzana ndi anthu.

Ngati mwaona kuti simukupeza bwino mu thupi lanu monga chimfine, mutu, kutentha thupi, musayendeyende khalani pakhomo mpaka muchire. Ngati muli ndi chimfine kapena mukubanika popuma thamangirani Ku chipatala.

Zikhulupiriro kapena mphekesera zokhudza Corona sibwino kuzitsata. Mwachitsanzo mphekesera zoti munthu womwa mowa sangadwale corona sibwino kumvera chifukwa tikhoza kufa nazo. Ngakhale uthenga wochokera kwa abwenzi athu kapena abale athu ukhoza kukhala wabodza. Nthawi zonse tiyeni titsatire zomwe azaumoyo akutilangiza mumadera athu.

Mukhoza kuthandiza kuchepetsa kufala kwa Corona pofalitsa uthengawu kwa anzanu komanso abale anu pogwiritsa ntchito whatsap ndi njira zinanso zofalitsira uthenga.

Uthengawu akukupatsirani ndi a bungwe lotchedwa Audiopedia.